Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 15:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo pomlola iwe acoke kwanu waufulu, musamamlola acoke wopanda kanthu;

14. mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.

15. Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.

16. Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17. pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18. Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.

19. Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa nchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 15