Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 12:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Musamadzacita monga mwa zonse tizicita kuno lero, yense kucita ciri conse ciyenera m'maso mwace;

9. pakuti mpaka lero simunafikira mpumulo ndi colowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.

10. Koma mudzaoloka Yordano, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.

11. Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.

12. Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.

13. Dzicenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 12