Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Tsidya lija la Yordano, m'dziko la Moabu, Mose anayamba kufotokozera cilamulo ici, ndi kuti.

6. Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebe, ndi kuti, Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;

7. bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kucidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwela, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebano, kufikira nyanja yaikuru Firate.

8. Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9. Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10. Yehova Mulungu wanu anakucurukitsani, ndipo taonani, lero mucuruka ngati nyenyezi za kumwamba.

11. Yehova Mulungu wa makolo anu, acurukitsire ciwerengero canu calero ndi cikwi cimodzi, nakudalitseni monga iye ananena nanu!

12. Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13. Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akuru anu.

14. Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwacita.

15. Potero ndinatenga akuru a mapfuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akuru anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mapfuko anu.

16. Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.

17. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akuru muwamvere m'modzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza ciweruzo nca Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18. Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzicita.

19. Pamenepo tinayenda ulendo kucokera ku Horebe, ndi kubzyola m'cipululu cacikuru ndi coopsa ciija conse munacionaci, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi Barinea.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1