Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.

17. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akuru muwamvere m'modzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza ciweruzo nca Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18. Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzicita.

19. Pamenepo tinayenda ulendo kucokera ku Horebe, ndi kubzyola m'cipululu cacikuru ndi coopsa ciija conse munacionaci, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi Barinea.

20. Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

21. Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamacita mantha, musamatenga nkhawa.

22. Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komweko, ndi za midzi yoti tidzafikako.

23. Ndipo cinandikomera cinthu ici; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri ainu, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;

24. amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku cigwa ca Esikolo, nacizonda.

25. Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m'manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.

26. Koma simunafuna kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.

27. Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, iye anatiturutsa m'dziko la Aigupto, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1