Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13. Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akuru anu.

14. Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwacita.

15. Potero ndinatenga akuru a mapfuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akuru anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mapfuko anu.

16. Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.

17. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akuru muwamvere m'modzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza ciweruzo nca Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18. Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzicita.

19. Pamenepo tinayenda ulendo kucokera ku Horebe, ndi kubzyola m'cipululu cacikuru ndi coopsa ciija conse munacionaci, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi Barinea.

20. Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

21. Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamacita mantha, musamatenga nkhawa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1