Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cacitatu ca Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Danieli, atatha kundionekera oyamba aja.

2. Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali m'Susani, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.

3. Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzace; yoposayo inaphuka m'mbuyo.

4. Ndinaona nkhosa yamphongo irikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwela; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pace; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lace; koma inacita monga mwa cifuniro cace, nidzikulitsa.

5. Ndipo polingirfrapo ine, taonani, wadza tonde wocokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ace.

6. Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona irikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yace yaukali.

7. Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, natyola nyanga zace ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pace, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lace.

8. Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukuru, koma atakhala wamphamvu, nyanga yace yaikuru inatyoka; ndi m'malo mwace munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza ku mphepo zinai za mlengalenga.

9. Ndipo mu imodzi ra izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukuru ndithu, kuloza kumwela, ndi kum'mawa, ndi ku dziko lokometsetsa.

10. Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza.

Werengani mutu wathunthu Danieli 8