Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 6:4-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola cifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza cifukwa kapena colakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona cosasamala kapena colakwa ciri conse mwa iye.

5. Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola cifukwa ciri conse Danieli amene, tikapanda kumtola ici pa cilamulo ca Mulungu wace.

6. Ndipo akuru awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo cikhalire.

7. Akuru onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lacifumu, ndi kuikapo coletsa colimba, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango,

8. Tsopano, mfumu, mukhazikitse coletsaco, ndi kutsimikiza colembedwaco, kuti cisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.

9. Momwemo mfumu Dariyo anatsimikiza colembedwa ndi coletsaco.

10. Ndipo podziwa Danieli kuti adatsimikiza colembedwaco, analowa m'nyumba mwace, m'cipinda mwace, cimene mazenera ace anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwadamaondo ace tsiku limodzi katatu, napemphera, nabvomereza pamaso pa Mulungu wace monga umo amacitira kale lonse.

11. Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Danieli alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wace.

12. Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za coletsaco ca mfumu, Kodi simunatsimikiza coletsaco, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Coona cinthuci, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.

13. Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena coletsa munacitsimikizaco; koma apempha pemphero lace katatu tsiku limodzi.

14. Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wace pa Danieli kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.

15. Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti coletsa ciri conse ndi lemba liri lonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.

16. Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Danieli, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Danieli, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

17. Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi cosindikizira cace, ndi cosindikizira ca akuru ace, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.

18. Pamenepo mfumu inamuka ku cinyumba cace, nicezera kusala usikuwo, ngakhale zoyimbitsa sanabwera nazo pamaso pace, ndi m'maso mwace munamuumira.

19. Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira ku dzenje la mikango.

20. Ndipo poyandikira padzenje inapfuula ndi mau acisoni mfumu, ninena, niti kwa Danieli, Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwamikango?

21. Pamenepo Danieli anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.

Werengani mutu wathunthu Danieli 6