Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 5:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pamenepo analowa naye Danieli kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Danieli, Ndiwe kodi Danieli uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?

14. Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.

15. Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace; koma sanakhoza kufotokozera kumasulira kwa cinthuci.

16. Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.

17. Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.

18. Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi cifumu;

19. ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.

20. Koma pokwezeka mtima wace, nulimba mzimu wace kucita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wace, namcotsera ulemerero wace;

21. ndipo anamuinga kumcotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wace unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pace mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira ali yense Iye afuna mwini.

22. Ndipo inu mwana wace, Belisazara inu, simunadzicepetsa m'mtima mwanu, cinkana munazidziwa izi zonse;

23. koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yace kwa inu; ndi inu ndi akuru anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolidi, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona, kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwace muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamcitira ulemu.

Werengani mutu wathunthu Danieli 5