Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 5:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mfumu Belisazara anakonzera anthu ace akulu cikwi cimodzi madyerero akuru, namwa vinyo pamaso pa cikwico.

2. Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golidi ndi siliva adazicotsa Nebukadinezara atate wace ku Kacisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akuru ace, akazi ace ndi akazi ace ang'ono, amweremo.

3. Nabwera nazo zotengera zagolidi adazicotsa ku Kacisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akuru ace, akazi ace ndi akazi ace ang'ono, anamweramo.

4. Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolidi, ndi yasiliva, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala.

5. Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa coikapo nyali, pomata pa khoma la cinyumba ca mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yace ya dzanja lidalembalo.

6. Pamenepo padasandulika pa nkhope pace pa mfumu, ndi maganizo ace anamsautsa, ndi mfundo za m'cuuno mwace zinaguruka, ndi maondo ace anaombana.

7. Nipfuulitsa mfumu abwere nao openda, Akasidi, ndi alauli, Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babulo, Ali yense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwace, adzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nadzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwu.

8. Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoza kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwace.

Werengani mutu wathunthu Danieli 5