Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa coikapo nyali, pomata pa khoma la cinyumba ca mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yace ya dzanja lidalembalo.