Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 4:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Cifukwa cace, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani macimo anu ndi kucita cilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kucitira aumphawi cifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.

28. Conseci cinagwera mfumu Nebukadinezara.

29. Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'cinyumba cacifumu ca ku Babulo.

30. Mfumu inanena, niti, Suyu Babulo wamkuru ndinammanga, akhale pokhala pacifumu, ndi mphamvu yanga yaikuru uoneke ulemerero wa cifumu canga?

31. Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ocokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakucokera.

32. Nadzakuinga kukucotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.

33. Nthawi yomweyo anacitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumcotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lace lidamera ngati nthenga za ciombankhanga ndi makadabo ace ngati makadabo a mbalame.

Werengani mutu wathunthu Danieli 4