Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 5:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israyeli, ndi kuti anakulitsa ufumu wace cifukwa ca anthu ace Israyeli.

13. Ndipo Davide anadzitengera akazi ang'ono ena ndi akazi a ulemu ena a ku Yerusalemu, atafikako kucokera ku Hebroni; ndipo anambadwira Davide ana amuna ndi akazi.

14. Maina a iwo anambadwira m'Yerusalemu ndi awa: Samua, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomo,

15. ndi Ibara ndi Elisua, ndi Nefegi ndi Yafiya;

16. ndi Elisama ndi Eliada ndi Elifeleti.

17. Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israyeli, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anacimva natsikira kungaka kuja.

18. Tsono Afilisti anafika natanda m'cigwa ca Refaimu.

19. Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.

20. Ndipo Davide anafika ku Baalaperazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baalaperazimu.

21. Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ace nawacotsa.

22. Ndipo Afilisti anakweranso kaciwiri, natanda m'cigwa ca Refaimu.

23. Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawaturukire pandunji pa mkandankhuku.

24. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova waturuka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.

25. Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezeri.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 5