Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 4:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwace; ndi Rekabu ndi Baana mbale wace anathawa.

7. Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali cigonere pakama pace m'cipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wace, nautenga namuka njira ya kucidikha usiku wonse,

8. Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera cilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Sauli ndi mbeu yace.

9. Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wace, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse,

10. muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Sauli wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilaga, ndiyo mphotho yace ndinampatsa cifukwa ca uthenga wace.

11. Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wace m'nyumba yace yace, ndidzafunsira mwazi wace ku dzanja lanu tsopano, ndi kukucotsani ku dziko lapansi?

12. Ndipo Davide analamulira anyamata ace, iwo nawapha, nawapacika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abineri ku Hebroni.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 4