Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Sauli, anamva kuti Abineri adakafera ku Hebroni, manja ace anafoka, ndi Aisrayeli onse anabvutika.

2. Ndipo Isiboseti, mwana wa Sauli anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lace Baana, ndi dzina la mnzace ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;

3. ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino.

4. Ndipo Jonatani mwana wa Sauli, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi, Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Sauli ndi Jonatani yocokera ku Jezreeli; ndipo mlezi wace adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lace ndiye Mefiboseti.

5. Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika ku nyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.

6. Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwace; ndi Rekabu ndi Baana mbale wace anathawa.

7. Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali cigonere pakama pace m'cipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wace, nautenga namuka njira ya kucidikha usiku wonse,

8. Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera cilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Sauli ndi mbeu yace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 4