Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 24:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndacimwa ine, ndinacita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.

18. Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Mjebusi.

19. Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova.

20. Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ace alikubwera kwa iye; naturuka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yace pansi.

21. Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide anati, Kugula dwale lako gi, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.

22. Arauna nati kwa Davide, Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe comkomera; sizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni;

23. zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni.

24. Koma mfumu inati kwa Arauna, lai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wace, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wace. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.

25. Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka cifukwa ca dziko, ndi mliri wa pa Israyeli unalekeka.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 24