Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 24:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha cimodzi ca izo, ndikakucitire cimeneco.

13. Comweco Gadi anafika kwa Davide, namuuza, nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupitikitsani miyezi itatu? kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Cenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.

14. Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zace nzazikuru; koma tisagwe m'dzanja la munthu.

15. Comweco Yehova anatumiza mliri pa Israyeli kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

16. Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lace ku Yerusalemu kuuononga, coipaco cinacititsa Yehova cisoni, iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Mjebusi.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 24