Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 20:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.

5. Comweco Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anacedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.

6. Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Seba mwana wa Bikri adzaticitira coipa coposa cija ca Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.

7. Ndipo anaturuka namtsata anthu a Yoabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onseamphamvu; naturuka m'Yerusalemu kukalondola Seba mwana wa Bikri.

8. Pamene anafika iwo pa mwala waukuru uli ku Gibeoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yoabu atabvala mwinjiro wace, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'cimace m'cuuno mwace; ndipo m'kuyenda kwace lidasololoka.

9. Ndipo Yoabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yoabu anagwira ndebvu za Amasa ndi dzanja lace lamanja kuti ampsompsone.

10. Koma Amasa sanasamalira lupanga liri m'dzanja la Yoabu; comweco iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ace pansi, osamgwazanso; nafa iye, Ndipo Yoabu ndi Abisai mbale wace analondola Seba mwana wa Bikri.

11. Ndipo mnyamata wina wa Yoabu anaima pali iye, nati, Wobvomereza Yoabu, ndi iye amene ali wace wa Davide, atsate Yoabu.

12. Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wace pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namcotsa pamseu kumka naye kuthengo, nampfunda ndi cobvala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 20