Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Seba mwana wa Bikri adzaticitira coipa coposa cija ca Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.