Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pacipata, Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu irikukhala pacipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisrayeli adathawa, munthu yense ku hema wace.

9. Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israyeli analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.

10. Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Cifukwa cace tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?

11. Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akuru a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu ku nyumba yace? pakuti mau a Aisrayeli onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo ku nyumba yace.

12. Inu ndinu abale anga, muli pfupa langa ndi mnofu wanga; cifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?

13. Ndipo munene ndi Amasa, Suli pfupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala cikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yoabu.

14. Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19