Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pacipata, Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu irikukhala pacipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisrayeli adathawa, munthu yense ku hema wace.