Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anauza Yoabu, Onani mfumu irikulira misozi, nilira Abisalomu.

2. Ndipo cipulumutso ca tsiku lila cinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu iri ndi cisoni cifukwa ca mwana wace.

3. Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kacetecete, monga azemba anthu akucita manyazi pakuthawa nkhondo.

4. Ndipo mfumu inapfunda nkhope yace, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga,

5. Ndipo Yoabu anafika ku nyumba ya mfumu, nati, Lero mwacititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu amuna ndi akazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono;

6. m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.

7. Cifukwa cace tsono nyamukani, muturuke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kuturuka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo cimeneci cidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19