Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 17:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.

17. Ndipo Jonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogeli; mdzakazi adafopita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi.

18. Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anacoka msanga onse awiri, nafika ku nyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali naco citsime pabwalo pace; ndipo anatsikira m'menemo.

19. Ndipo mkazi anatenga cibvundikilo naciika pakamwa pa citsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sicinadziwika.

20. Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Jonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kumka ku Yerusalemu.

21. Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anaturuka m'citsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofeli anapangira zotere pa inu.

22. Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordano. Kutaca m'mawa sanasowa mmodzi wa iwo wosaoloka Yordano.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 17