Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anaturuka m'citsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofeli anapangira zotere pa inu.