Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:29-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Cifukwa cace Zadoki ndi Abyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.

30. Ndipo Davide anakwera pa cikweza ca ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anapfunda mutu wace nayenda ndi mapazi osabvala; ndi anthu onse amene anali naye anapfunda munthu yense mutu wace, ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

31. Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofeli ali pakati pa opangana ciwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.

32. Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai M-ariki anadzakomana naye ali ndi maraya ace ong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

33. Ndipo Davide ananena naye, Ukapita pamodzi ndi ine udzandilemetsa;

34. koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofeli.

35. Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abyatara ansembewo kodi? motero ciri conse udzacimva ca m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abyatara ansembewo.

36. Onani, ali nao komweko ana amuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Jonatani mwana wa Abyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze ciri conse mudzacimva.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15