Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Jonatani mwana wa Abyatara.

28. Ona ndidzaima pa madooko a m'cipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.

29. Cifukwa cace Zadoki ndi Abyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.

30. Ndipo Davide anakwera pa cikweza ca ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anapfunda mutu wace nayenda ndi mapazi osabvala; ndi anthu onse amene anali naye anapfunda munthu yense mutu wace, ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

31. Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofeli ali pakati pa opangana ciwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.

32. Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai M-ariki anadzakomana naye ali ndi maraya ace ong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

33. Ndipo Davide ananena naye, Ukapita pamodzi ndi ine udzandilemetsa;

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15