Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:22-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ace onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye.

23. Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kucipululu.

24. Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la cipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kuturuka m'mudzimo.

25. Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwererenalo likasa la Mulungu kumudziko; akandikomera mtima Yehova, iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso gi, ndi pokhala pace pomwe.

26. Koma iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andicitire cimene cimkomera.

27. Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Jonatani mwana wa Abyatara.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15