Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.

15. Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

16. Mfumu nituruka, ndi banja lace lonse tinamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi ang'ono, kusunga nyumbayo.

17. Ndipo mfumu inaturuka, ndi anthu onse anamtsata; naima ku nyumba ya payokha.

18. Ndipo anyamata ace onse anapita naye limodzi; ndi Akereri ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kucokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.

19. Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.

20. Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? ubwerere nubwereretsenso abale ako; cifundo ndi zoonadi zikhale nawe.

21. Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15