Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 14:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine ali yense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.

11. Nati iye, Mfumu mukumbukile Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.

12. Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti Iyo, Nena.

13. Ndipo mkaziyo anati, Cifukwa ninjinso munalingalira cinthu cotere pa anthu a Mulungu? pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga woparamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wace.

14. Pakuti kufa tidzafa, ndipo tiri ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sacotsa moyo, koma alingalira ngra yakuti wotayikayo asakhale womtayikira iye.

15. Cifukwa cace tsono cakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndico kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzacita copempha mdzakazi wace.

16. Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wace m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kuticotsa ku colowa ca Mulungu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 14