26. Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Amnoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, iye apitirenji nawe?
27. Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Amnoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye.
28. Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ace, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Amnoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Amnoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, citani camuna.
29. Ndipo anyamata a Abisalomu anamcitira Amnoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yace, nathawa.
30. Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense.
31. Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zobvala zace nigona pansi, ndipo anyamata ace onse anaimirirapo ndi zobvala zao zong'ambika.