Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 13:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali citapita ici, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wace wokongola, dzina lace ndiye Tamara, Amnoni mwana wa Davide anamkonda iye.

2. Ndipo Amnoni anapsinjikadi nayamba kudwala cifukwa ca mlongo wace Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Amnoni anaciyesa capatali kumcitira kanthu.

3. Koma Amnoni anali ndi bwenzi lace, dzina lace ndiye Jonadabu, mwana wa Sineya, mbale wa Davide. Ndipo Jonadabu anali munthu wocenjera ndithu.

4. Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Amnoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.

5. Ndipo Jonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomeza ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere cakudyaco pamaso panga kuti ndicione ndi kucidya ca m'manja mwace.

6. Comweco Amnoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Amnoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye ca m'manja mwace.

7. Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite ku nyumba ya mlongo wako Amnoni, numkonzere cakudya,

8. Comweco Tamara anapita ku nyumba ya mlongo wace Amnoni; ndipo iye anali cigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pace, nakazinga timitandato.

9. Ndipo anatenga ciwaya natiturutsa pamaso pace; koma anakana kudya. Ndipo Amnoni anati, Anthu onse aturuke kundisiya ine. Naturuka onse, kumsiya.

10. Ndipo Amnoni anati kwa Tamara, Bwera naco cakudya kucipinda kuti ndikadye ca m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kucipinda kwa Amnoni mlongo wace.

11. Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.

12. Koma iye anamyankha nati, lai, mlongo wanga, usandicepetsa ine, pakuti cinthu cotere siciyenera kucitika m'Israyeli, usacita kupusa kumeneku.

13. Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israyeli. Cifukwa cace tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.

14. Koma iye sadafuna kumvera mau ace, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkangamiza, nagona naye.

15. Atatero Amnoni anadana naye ndi cidani cacikuru kopambana; pakuti cidani cimene anamuda naco, cinali cacikuru koposa cikondi adamkonda naco. Ndipo Amnoni ananena naye, Nyamuka, coka.

16. Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti coipa ici cakuti ulikundipitikitsa ncacikuru coposa cina cija unandicitira ine. Kama anakana kumvera.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 13