Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 12:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.

17. Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.

18. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?

19. Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

20. Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.

21. Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,

22. Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandicitira cifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.

23. Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.

24. Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wace, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Solomo. Ndipo Yehova anamkonda iye,

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 12