Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 11:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Davide anatumiza Yoabu, pamodzi ndi anyamata ace, ndi Aisrayeli onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsaliraku Yerusalemu.

2. Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wace nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wocititsa kaso pomuyang'ana.

3. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?

4. Ndipo bavide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adacoka mumsambo; ndipo anabwereranso ku nyumba yace.

5. Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti, Ndiri ndi pakati.

6. Davide natumiza kwa Yoabu, nati, Unditumizire Uriya Mhiti. Ndipo Yoabu anatumiza Uriya kwa Davide.

7. Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yoabu ali bwanji? ndi anthu ali bwanji? ndi nkhondo iri bwanji?

8. Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire ku nyumba yako, nutsuke mapazi ako, Ndipo Uriya anacoka ku nyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.

9. Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wace, osatsikira ku nyumba yace.

10. Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsildra ku nyumba yace, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? cifukwa ninji sunatsikira ku nyumba yako?

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 11