Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 10:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Comweco Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndebvu zao mbali imodzi, nadula zobvala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.

5. Pamene anaciuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anacita manyazi akuru. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndebvuzanu; zitameramubwere.

6. Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

7. Ndipo pamene Davide anacimva, anatumiza Yoabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu.

8. Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo polowera kucipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 10