Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 9:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo, anadza kumuyesera Solomo ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukuru, ndi ngamila zosenza zonunkhira, ndi golidi wocuruka, ndi timiyala ta mtengo wace; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.

2. Ndipo Solomo anammasulira mau ace onse, panalibe kanthu kombisikira Solomo, kamene sanammasulira.

3. Ndipo mfumu yaikazi ya ku Seba ataiona nzeru ya Solomo, ndi nyumba adaimanga,

4. ndi zakudya za pa gome lace, ndi makhalidwe a anyamata ace, ndi maimiriridwe a atumiki ace, ndi mabvalidwe ao, ndi otenga zikho ace, ndi mabvalidwe ao, ndi makweredwe ace pokwera iye kumka ku nyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

5. Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya macitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.

6. Koma sindinakhulupira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zocuruka; mwa, onjezatu pa mbiri ndidaimva.

7. Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima ciimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.

8. Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wace, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ace; popeza Mulungu wanu anakonda Aisrayeli kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kucita ciweruzo ndi cilungamo.

9. Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wace; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Seba anapatsa mfumu Solomo.

10. Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomo otenga golidi ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.

11. Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oyimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.

12. Ndipo mfumu Solomo anampatsa mfumu yaikazi ya ku Seba cifuniro cace conse, ciri conse anacipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lace, iyeyu ndi anyamata ace.

13. Kulemera kwace tsono kwa golidi anafika kwa Solomo caka cimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi;

14. osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golidi ndi siliva kwa Solomo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 9