Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 7:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Solomo anapatula pakati pace pa bwalo liri pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomo linacepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

8. Nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, khamu lalikuru ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Aigupto.

9. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu anacita msonkhano woletsa; popeza anacita zakupereka guwa la nsembe masiku asanu ndi awiri, ndi madyerero masiku asanu ndi awiri.

10. Ndipo tsiku la makumi awiri ndi citatu la mwezi wacisanu ndi ciwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao cifukwa ca zokoma Yehova adawacitira Davide, ndi Solomo, ndi Aisrayeli anthu ace.

11. Momwemo Solomo anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo ziri zonse zidalowa mumtima mwace mwa Solomo kuzicita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yace yace, anacita mosabwezeza.

12. Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomo usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.

13. Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 7