Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 7:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atatha tsono Solomo kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi.

2. Ndipo ansembe sanakhoza kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

3. Ndi ana onse a Israyeli anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire.

4. Pamenepo mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.

5. Ndipo mfumu Solomo anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi, makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Yehova.

6. Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoyimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala ciriri Israyeli yense.

7. Ndipo Solomo anapatula pakati pace pa bwalo liri pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomo linacepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

8. Nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, khamu lalikuru ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Aigupto.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 7