Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 6:30-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera ali yense monga mwa njira zace zonse, monga mudziwa mtima wace; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;

31. kuti aope Inu, kuyenda m'njira zanu masiku onse akukhala iwo m'dziko limene munapatsa makolo athu.

32. Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israyeli, akafumira ku dziko lakutari cifukwa ca dzina lanu lalikuru, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono wanu wotambasuka; akadza iwowa ndi kupemphera kuloza ku nyumba iyi;

33. pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumcitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisrayeli; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi ichedwa ndi dzina lanu.

34. Akaturukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iri yonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza ku mudzi uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;

35. pamenepo mumvere m'Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

36. Akacimwira Inu (pakuti palibe munthu wosacimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kumka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi;

37. koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tacimwa, tacita mphulupulu, tacita coipa;

38. akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m'dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mudzi mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;

39. pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao; nimukhululukire anthu anu amene anakucimwirani.

40. Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale cipenyere, ndi makutu anu cimvere, pemphero locitika pamalo pano.

41. Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, abvale cipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 6