Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 35:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.

15. Ndi oyimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera

16. Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kucita Paskha, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.

17. Ndipo ana a Israyeli okhalako anacita Paskha nthawi yomweyo, ndi madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri.

18. Panalibe Paskha wocitika m'Israyeli wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samueli mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israyeli anacita Paskha wotere, ngati ameneyu anacita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisrayeli opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.

19. Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anacita Paskha amene.

20. Citatha ici conse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aigupto anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Firate; ndipo Yosiya anamturukira kuyambana naye.

21. Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndiri ndi ciani ndi inu, mfumu ya Yuda? sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndiri nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kubvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.

22. Koma Yosiya sanatembenuka nkhope yace kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ocokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'cigwa ca Megido.

23. Ndipo oponya anayang'anitsa mibvi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ace, Ndicotseni ndalasidwa ndithu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 35