Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 30:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatula; potero Alevi anayang'anira kupha za Paskha kwa ali yense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.

18. Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efraimu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretsa, koma anadya Paskha mosati monga munalembedwa.

19. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wace kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ace, cinkana sanayeretsedwa monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.

20. Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawaciritsa anthu.

21. Ndipo ana a Israyeli opezeka m'Yerusalemu anacita madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe cacikuru; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoyimbira zakuliritsa kwa Yehova.

22. Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.

23. Ndipo msonkhano wonse unapangana kucita masiku asanu ndi awiri ena, nacita masiku asanu ndi awiri ena ndi cimwemwe.

24. Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akuru anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembeambiri adadzipatula,

25. Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wocokera kwa Israyeli, ndi alendo ocokera ku dziko la Israyeli, ndi okhala m'Yuda, anakondwera.

26. Momwemo munali cimwemwe cacikuru m'Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli simunacitika cotero m'Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 30