Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 28:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lace,

2. koma anayenda m'njira za mafumu a Israyeli, napangiranso Abaala mafano oyenga,

3. Nafukizanso yekha m'cigwa ca mwana wa Hinomu, napsereza ana ace m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israyeli.

4. Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira.

5. Cifukwa cace Yehova Mulungu wace anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukuru wa anthu ace, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israyeli, amene anamkantha makanthidwe akuru.

6. Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.

7. Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efraimu anapha Maseya mwana wa mfumu, ndi Azrikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.

8. Ndipo ana a Israyeli anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana amuna ndi akazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya,

9. Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lace Odedi; naturuka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 28