Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 26:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ciwerengo conse ca akuru a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndico zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.

13. Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ocita nkhondo ndi mphamvu yaikuru, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.

14. Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zacitsulo, ndi maraya acitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.

15. Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungondya, aponye nao mibvi ndi miyala yaikuru. Ndi dzina lace linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwiza, mpaka analimbikatu.

16. Koma atakhala wamphamvu, mtima wace unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wace; popeza analowa m'Kacisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la cofukiza.

17. Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pace, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima;

18. natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova, koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; turukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.

19. Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza iri m'dzanja lace kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pace, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.

20. Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pace namkankhiza msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kuturukako, pakuti Yehova adamkantha.

21. Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa ku nyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wace anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.

22. Macitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amosi. Ndipo Uziya anagona ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 26