Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 25:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani, tionane maso.

18. Ndi Yoasi mfumu ya Israyeli anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebano inapitapo, nipondereza mtungwi.

19. Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.

20. Koma wosamvera Amaziya, pakuti nca Mulungu ici kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.

21. Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.

22. Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israyeli, nathawa yense kuhema kwace.

23. Ndipo Yoasi mfumu ya Israyeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yoasi mwana wa Yehoahazi, ku Betisemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira cipata ca Efraimu kufikira cipata ca kungondya, mikono mazana anai.

24. Natenga golidi ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obedi Edomu, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwerera kumka ku Samariya.

25. Ndipo Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yoasi mwana wa Yehoahazi mfumu ya Israyeli, zaka khumi ndi zisanu.

26. Macitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, salembedwa kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli?

27. Ndipo cipambukire Amaziya kusatsata Yehova, anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.

28. Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Yuda.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 25