Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 24:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkuru wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kucokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israyeli, ukhale wa cihema ca umboni?

7. Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola citseko ca nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.

8. Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja ku cipata ca nyumba ya Yehova.

9. Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisrayeli m'cipululu.

10. Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha.

11. Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinacurukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhutula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwace. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zocuruka.

12. Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira nchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akucita ndi citsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.

13. Momwemo anacita ogwira nchito, nikula nchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ace, nailimbitsa.

14. Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golidi ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

15. Koma Yehoyada anakalamba, nacuruka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.

16. Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anacita zabwino m'Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yace.

17. Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.

18. Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, cifukwa ca kuparamula kwao kumene.

19. Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawacitira umboni; koma sanawamvera.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 24