Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 21:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikuru, za siliva, ndi za golidi, ndi za mtengo wace, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wace woyamba.

4. Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wace, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ace onse, ndi akalonga ena omwe a Israyeli,

5. Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.

6. Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, umo anacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wace; ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova.

7. Koma Yehova sanafuna kuononga nyumba ya Davide cifukwa ca pangano adalicita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ace nyali nthawi zonse.

8. Masiku ace Aedomu anapanduka kucoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.

9. Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ace, ndi magareta ace onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magareta,

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 21