Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 14:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7. Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosabvutika.

8. Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.

9. Ndipo anawaturukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi cikwi cimodzi, ndi magareta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

10. Naturuka Asa pamaso pace, nanika nkhondoyi m'cigwa ca Sefata ku Maresa.

11. Ndipo Asa anapfuulira kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, taturukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakulakeni.

12. Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.

13. Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ace; ndipo anatenga zofunkha zambiri.

14. Ndipo anakantha midzi yonse pozungulira pace pa Gerari; a pakuti mantha ocokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'midzi monse, pakuti mudacuruka zofunkha m'menemo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 14