Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 12:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pamenepo akalonga a Israyeli ndi mfumu anadzicepetsa, nati, Yehova ali wolungama.

7. Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzicepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzicepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa cipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisaki.

8. Koma adzakhala akapolo ace, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.

9. Ndipo Sisaki mfumu ya Aigupto anakwerera Yerusalemu, nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; anazicotsa zonse; anacotsanso zikopa zagolidi adazipanga Solomo.

10. Ndipo Rehabiamu mfumu anapanga m'malo mwa izo zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11. Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku cipinda ca olindirira.

12. Ndipo pakudzicepetsa iye mkwiyo wa Mulungu unamcokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma m'Yuda.

13. Nadzilimbitsa Rehabiamu mfumu m'Yerusalemu, nacita ufumu; pakuti Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli, kuikapo dzina lace; ndipo dzina la mace ndiye Naama M-amoni.

14. Koma anacita coipa, popeza sanalunjikitsa mtima wace kufuna Yehova.

15. Macitidwe ace tsono a Rehabiamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizilembedwa kodi m'buku la mau a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku onse.

16. Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide; ndipo Abiya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 12