Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 9:18-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.

19. Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.

20. Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimsi, pakuti ayendetsa moyaruka.

21. Nati Yoramu, Manga. Namanga gareta wace, Ndipo Yoramu mfumu ya Israyeli ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anaturuka yense m'gareta wace, naturuka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezreeli.

22. Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anari, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala cacuruka cigololo ndi nyanga zace za mai wako Yezebeli?

23. Natembenuza Yoramu manja ace, nathawa, nati kwa Ahaziya, Ciwembu, Ahaziya.

24. Nafa nao Yehu uta wace, nalasa Yoramu pacikota, nuturuka mubvi pa mtima wace, naonyezeka iye m'gareta wace.

25. Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wace, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezreeli; pakuti kumbukila m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wace, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.

26. Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ace, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova, Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.

27. Koma pociona ici Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku khumbi la m'munda. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagareta; namkantha pa cikweza ca Guru ciri pafupi pa Yibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.

28. Ndipo anyamata ace anamnyamulira pagareta kumka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ace pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

29. Ndipo pa caka cakhumi ndi cimodzi ca Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.

30. Ndipo pofika Yehu ku Yezreeli, Yezebeli anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lace, nasuzumira pazenera.

31. Ndipo polowa Yehu pacipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimri, iwe wakupha mbuyako?

32. Koma anakweza maso ace kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.

33. Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wace pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.

34. Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

35. Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezako kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 9