Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 9:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine cakuti cakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israyeli.

13. Nafulumira iwo, nagwira yense copfunda cace, naciyala pokhala iye paciunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.

14. Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Gileadi, iye ndi Aisrayeli onse, cifukwa ca Hazaeli mfumu ya Aramu;

15. koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezreeh ampoletse mabala ace anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kuturuka m'mudzi kukafotokozera m'Yezreeli.

16. Nayenda Yehu m'gareta, namuka ku Yezreeli, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu.

17. Ndipo mlonda ali ciriri pacilindiro m'Yezreeli, naona gulu la Yehu lirinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi?

18. Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.

19. Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.

20. Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimsi, pakuti ayendetsa moyaruka.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 9