Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 6:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu paticepera

2. Mutilole tipite ku Yordano, tikatengeko, ali yense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo, Nati, Mukani.

3. Ndipo wina anati, Mulole mupite nafe anyamata anu. Nati, Ndidzamuka.

4. Namuka nao, nafika ku Yordano, iwo natema mitengo.

5. Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anapfuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! popeza ojobwereka.

6. Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.

7. Nati, Katole. Natambasula dzanja lace, naitenga.

8. Ndipo mfumu ya Aramu inalinkucita nkhondo ndi Israyeli, nipangana ndi anyamata ace, kuti, Misasa yanga idzakhala pakuti pakuti.

9. Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Mucenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.

10. Pamenepo mfumu ya Israyeli inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumcenjeza; nadzisunga osapitako, kawiri kawiri.

11. Koma mtima wa mfumu ya Aramu unabvutika kwambiri pa icico, naitana anyamata ace, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wobvomerezana ndi mfumu ya Israyeli ndani?

12. Nati mmodzi wa anyamata ace, lai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israyeli, ndiye amafotokozera mfumu ya Israyeli mau muwanena m'kati mwace mwa cipinda canu cogonamo.

13. Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotana.

14. Pamenepo anatumizako akavalo ndi magareta ndi khamu lalikuru, nafikako usiku, nauzinga mudziwo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 6