Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 5:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.

11. Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.

12. Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israyeli? ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nacoka morunda.

13. Pamenepo anyamata ace anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani cinthu cacikuru, simukadacicita kodi? koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?

14. Potero anatsika, namira m'Yordano kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wace unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.

15. Pamer nepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lace lonse, nadzaima pamaso pace, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israyeli ndiko; ndipo tsopano, mulandire cakukuyamikani naco kwa mnyamata wanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 5